8. Ndipo wacinai anatsanulira mbale yace padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto.
9. Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukuru; ndipo anacitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amcitire ulemu.
10. Ndipo wacisanu anatsanulira mbale yace pa mpando wacifumu wa cirombo; ndipo ufumu wace unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwace,
11. nacitira mwano Mulungu wa m'Mwamba cifukwa ca zowawa zao ndi zironda zao; ndipo sanalapa nchito zao.
12. Ndipo wacisanu ndi cimodzi anatsanulira mbale yace pa mtsinje waukuru Firate; ndi madzi ace anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ocokera poturuka dzuwa.