12. Ndipo wacisanu ndi cimodzi anatsanulira mbale yace pa mtsinje waukuru Firate; ndi madzi ace anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ocokera poturuka dzuwa.
13. Ndipo ndinaona moturuka m'kamwa mwa cinjoka, ndi m'kamwa mwa cirombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati acule;
14. pakuti ali mizimu ya ziwanda zakucita zizindikilo; zimene zituruka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikuru la Mulungu, Wamphamvuyonse.
15. (Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zobvala zace, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wace.)
16. Ndipo anawasonkhanitsira ku malo ochedwa m'Cihebri Harmagedo.