7. komatu m'masiku a mau a mngelo wacisanu ndi ciwiri m'mene iye adzayamba kuomba, pamenepo padzatsirizika cinsinsi ca Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ace aneneri.
8. Ndipo mau ndinawamva ocokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalom'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.
9. Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimbamwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uci.
10. Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uci; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.
11. Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.