16. Cotero sicifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene acitira cifundo.
17. Pakuti lembo linena kwa Farao, Cifukwa ca ici, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.
18. Cotero iye acitira cifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuumitsamtima.
19. Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza cifuno cace?
20. Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi cinthu copangidwa cidzanena ndi amene anacipanga, U ndipangiranji ine cotero?
21. Kodi kapena woumba mbiya sakutha kucita zace padothi, kuumba ndi ncinci yomweyo cotengera cimodzi caulemu ndi cina camanyazi?