1. Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.
2. Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.
3. Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;
4. kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.
5. Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: