Aroma 6:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?

17. Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;

18. ndipo pamene munamasulidwa kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo,

19. Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.

20. Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira cilungamo.

21. Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.

Aroma 6