Aroma 2:27-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa cibadwidwe, ngati kukwanira cilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo?

28. Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo;

29. koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwace sikucokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.

Aroma 2