19. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.
20. Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.
21. Timoteo wanchito mnzanga akulankhulani inu; ndi Lukiyo ndi Yasoni ndi Sosipatro, abale anga.