Aroma 15:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.

7. Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.

8. Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,

9. ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa ca cifundo; monga kwalembedwa,Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,Ndidzayimbira dzina lanu.

10. Ndiponso anena,Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.

11. Ndiponso,Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse;Ndipo anthu onse amtamande.

12. Ndiponso, Yesaya ati,Padzali muzu wa Jese,Ndi iye amene aukira kucita ufumu pa anthu amitundu;Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.

Aroma 15