1. Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
2. Yense wa ife akondweretse mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa.
3. Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe Inagwa pa Ine,
4. Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.