28. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;
29. anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, cinyengo, udani;
30. akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, acipongwe, odzitama, amatukutuku, ovamba zoipa, osamvera akuru ao,
31. opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda cikondi ca cibadwidwe, opanda cifundo;
32. amene ngakhale adziwa kuweruza kwace kwa Mulungu, kuti iwo 2 amene acita zotere ayenera imfa, azicita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzicita.