19. cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.
20. Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
21. cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,
22. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;
23. nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi cifaniziro ca munthu woonongeka ndi ca mbalame, ndi ca nyama zoyendayenda, ndi ca zokwawa.