11. Pakuti atero Amosi, Yerobiamu adzafa ndi lupanga, ndi Israyeli adzatengedwadi ndende, kucoka m'dziko lace.
12. Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, coka, thawira ku dziko la Yuda, nudye, nunenere komweko;
13. koma usaneneranso ku Beteli; pakuti pamenepo mpa malo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yacifumu.
14. Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakuchera nkhuyu;
15. ndipo Yehova ananditenga ndirikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israyeli.