4. Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israyeli, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;
5. koma musamafuna Beteli, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Beteli adzasanduka cabe.
6. Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi mayo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Beteli;
7. inu osintha ciweruzo cikhale civumulo, nimugwetsa pansi cilungamo,
8. Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova;
9. wakufikitsa cionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, cionongeko nicigwera linga,
10. Iwo adana naye wodzudzula kucipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.
11. Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wace.