Amosi 5:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova! mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? ndilo mdima, si kuunika ai.

19. Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi cimbalangondo cikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lace, nimluma njoka.

20. Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

21. Ndidana nao, ndinyoza madyerero anu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa.

22. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndinsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.

23. Mundicotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu.

Amosi 5