1. Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basana, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani naco, timwe.
2. Ambuye Yehova walumbira pali ciyero cace, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakucotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3. Ndipo mudzaturukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwace, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4. Idzani ku Beteli, mudzalakwe ku Giligala, nimucurukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatu atatu;
5. nimutenthe nsembe zolemekeza zacotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ici mucikonda, inu ana a Israyeli, ati Ambuye Yehova.