1. Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basana, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani naco, timwe.
2. Ambuye Yehova walumbira pali ciyero cace, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakucotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3. Ndipo mudzaturukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwace, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.