7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:
9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,
10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;
11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.