5. Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;
6. cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:
9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,
10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;
11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
12. Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;
13. kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
14. koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.
15. Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
16. Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.