1. PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,
2. kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Kristu a m'Kolose: Cisomo kwa inu ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu.
3. Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi kupempherera Inu nthawi zonse,
4. popeza tidamva za cikhulupiriro canu ca mwa Kristu Yesu, ndi cikondi muli naco kwa oyera mtima onse;