8. Mudagonjetsa zonse pansi pa mapaziace.Pakuti muja adagonietsa zonse kwa iye, sanasiyapo kanthu kosamgoniera iye. Koma sitinayamba tsopano apa kuona zonse zimgonjera.
9. Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.
10. Pakuti kunamuyenera iye amene zonse ziri cifukwa ca iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa cipulumutso cao mwa zowawa.