3. Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ocimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.
4. Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo cimo;
5. ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana,Mwana wanga, usayese copepuka kulanga kwa Ambuye,Kapena usakomoke podzudzulidwa ndilye;
6. Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga,Nakwapula mwana ali yense amlandira.
7. Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu acitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wace wosamlanga?
8. Koma ngati mukhala opanda cilango, cimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.
9. Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?