14. Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.
15. Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16. Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17. Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;
18. amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa: