31. 3 Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.
32. Koma tadzikumbursani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa 4 mudapirira citsutsano cacikuru ca zowawa;
33. pena pocitidwa 5 cinthu cooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ocitidwa zotere.
34. Pakuti 6 munamva cifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa cuma canu, 7 pozindikira kuti muli naco nokha cuma coposa caeikhalire.
35. Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli naco cobwezera mphotho cacikuru.