23. tigwiritse cibvomerezo cosagwedera ca ciyembekezo cathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
24. ndipo tiganizirane wina ndi mnzace kuti tifulumizane ku cikondano ndi nchito zabwino,
25. osaieka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika.
26. Pakuti tikacimwa ife eni ace, titatha kulandira cidziwitso ca coonadi, siitsalanso nsembe ya kwa macimo,
27. koma kulindira kwina koopsa kwa ciweruziro, ndi kutentha kwace kwa mota wakuononga otsutsana nao.