Agalatiya 6:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta.

8. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m'thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

9. Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

10. Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.

11. Taonani, malembedwe akuruwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.

12. Onseamene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu.

Agalatiya 6