11. Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.
12. Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu Kristu.
13. Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Ciyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,
14. ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Ciyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wacangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
15. Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa cisomo cace,