14. Citani zonse kopanda madandaulo ndi makani,
15. kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda cirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
16. akuonetsera mau a movo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira: nao m'tsiku la Kristu, kuti sindinathamanga cabe, kapena kugwiritsa nchito cabe.
17. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
18. momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.