22. Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi, ndiko cipatso ca nchito yanga, sindizindikiranso cimene ndidzasankha.
23. Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala naco colakalaka ca kucoka kukhala ndi Kristu, ndiko kwabwino koposa-posatu;
24. koma kukhalabe m'thupi ndiko kufunika koposa, cifukwa ca inu.
25. Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezeracimwemwe ca cikhulupiriro canu;
26. kuti kudzitamandira kwanu kucuruke m'Kristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.
27. Cokhaci, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Kristu: kuti, ndingakhale nditi ndirinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva za kwa inu, kuti mucirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi cikhulupiriro ca Uthenga Wabwino;
28. osaopa adani m'kanthu konse, cimene ciri kwa iwowa cisonyezo ca cionongeko, koma kwa inu ca cipulumutso, ndico ca kwa Mulungu;
29. kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu cifukwa ca Kristu, si kukhulupirira kwa iye kokha, komatunso kumva zowawa cifukwa ca iye,