Aefeso 5:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pace, pakuti cifukwa ca hi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7. Cifukwa cace musakhale olandirana nao;

8. pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9. pakuti cipatso ca kuunika ticipeza m'ubwino wonse, ndi cilungamo, ndi coonadi,

10. kuyesera cokondweretsa Ambuye nciani;

11. ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse;

Aefeso 5