Aefeso 5:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

27. kutilye akadziikire yekha Eklesia wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda cirema.

28. Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29. pakuti munthu sanadana nalo thupi lace ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia;

30. pakuti tiri ziwalo za thupi lace.

31. 1 Cifukwa ca ici munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wace; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

Aefeso 5