15. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;
16. akucita macawi, popeza masiku ali oipa,
17. Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.
18. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu,
19. ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;
20. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;
21. ndi kumverana wina ndi mnzace m'kuopa Kristu.