Aefeso 4:22-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;

23. koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

24. 2 nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca coonadi.

25. Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.

Aefeso 4