4. monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,
5. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace,
6. kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.
7. Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,
8. cimene anaticurukitsira ife m'nzeru zonse, ndi cisamaliro.
9. Anatizindikiritsa ife cinsinsi ca cifuniro cace, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa iye,