Aefeso 1:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. kuti ife amene dnakhulupirira Kristu kale tikayamikitse ulemerero wace.

13. Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

14. ndiye cikole ca colowa cathu, kuti ace ace akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wace uyamikike.

Aefeso 1