7. pakuti cifukwa ca dzinali anaturuka, osalandira kanthu kwa amitundu.
8. Cifukwa cace ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana naco coonadi,
9. Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkuru wa iwo, satilandira ife.