1. MKURUYO kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ace, amene ine ndikondana nao m'coonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira coonadi;
2. cifukwa ca coonadi cimene cikhala mwa ife, ndipo cidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:
3. Cisomo, cifundo, mtendere zikhale ndi ife zocokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Kristu Mwana wa Atate, m'coonadi ndi m'cikondi.
4. Ndakondwera kwakukuru kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'coonadi, monga tinalandira lamulo locokera kwa Atate.