15. ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira cipulumutso, mwa cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.
16. Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:
17. kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kucita nchito iri yonse yabwino.