2 Samueli 6:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?

10. Momwemo Davide sanafuna kudzitengera likasa la Yehova lidze ku mudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.

11. Ndipo a likasa la Yehova linakhala m'nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa Obedi-Edomu ndi banja lace lonse.

12. Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obedi-Edomu ndi zace zonse, cifukwa ca likasa la Mulungu. Comweco Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu, nakwera nalo ku mudzi wa Davide, ali ndi cimwemwe.

2 Samueli 6