8. Ndipo tsiku lija Davide anati, Ali yense akakantha Ajebusi, aponye m'madzi opuala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Cifukwa cace akuti, Akhungu ndi opuala sangalowe m'nyumbamo.
9. Ndipo Davide anakhala m'linga mula, nalicha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.
10. Ndipo Davide anakula cikulire cifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.
11. Ndipo Hiramu mfumu ya Turo anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.