16. ndi Elisama ndi Eliada ndi Elifeleti.
17. Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israyeli, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anacimva natsikira kungaka kuja.
18. Tsono Afilisti anafika natanda m'cigwa ca Refaimu.
19. Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.
20. Ndipo Davide anafika ku Baalaperazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baalaperazimu.
21. Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ace nawacotsa.
22. Ndipo Afilisti anakweranso kaciwiri, natanda m'cigwa ca Refaimu.