2 Samueli 23:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;

21. ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22. Izi anacita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23. Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ace.

2 Samueli 23