17. Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;
18. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,
19. Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga,
20. Iye ananditurutsanso ku malo akuru;Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.