11. Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,
12. Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye,Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.
13. Ceza ca pamaso paceMakala a mota anayaka,
14. Yehova anagunda kumwamba;Ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ace.
15. Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;Mphezi, nawaopsa,
16. Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,Maziko a dziko anaonekera poyera,Ndi mthonzo wa Yehova,Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.
17. Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;
18. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,