2 Samueli 20:23-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo Yoabu anali woyang'anira khamu lonse la Israyeli; ndi Benaya, mwana wa Jehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;

24. ndi Adoramu anayang'anira msonkho; ndi Jehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri;

25. ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abyatara anali ansembe;

26. ndiponso Ira Mjairi anali nduna ya Davide.

2 Samueli 20