13. Atamcotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumsata Yoabu kukalondola Seba mwana wa Bikri.
14. Ndipo anapyola mapfuko onse a Israyeli kufikira ku Abeli ndi ku Betimaaka, ndi kwa Aberi onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.
15. Ndipo anadza nammangira misasa m'Abeli wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda tioga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yoabu anakumba lingalo kuti aligwetse.
16. Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mudzimo anapfuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yoabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndgankhule nanu.