13. ocitidwa zoipa kulipira kwa cosalungama; anthu akuyesera cowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zirema, akudyerera m'madyerero acikondi ao, pamene akudya nanu;
14. okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
15. posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya cosalungama;
16. koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwace mwini; buru wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyarukakwa mneneriyo.