2 Mbiri 6:41-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, abvale cipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.

42. Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukile zacifundo za Davide mtumiki wanu.

2 Mbiri 6