1. Pamenepo Solomo anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani.
2. Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.
3. Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yace, nidalitsa khamu lonse la Israyeli; ndi khamu lonse la Israyeli linaimirira.
4. Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, wakunena m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa: ndi manja ace, ndi kuti,