2 Mbiri 5:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Nadza akulu akulu onse a Israyeli, nanyamula likasalo Alevi.

5. Ndipo anakwera nalo likasa, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'cihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.

6. Ndi mfumu Solomo ndi khamu lonse la Israyeli losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kucuruka kwace.

7. Ndipo ansembe analowa nalo likasa la cipangano la Yehova kumalo kwace m'moneneramo mwa kacisi, m'malo opatulikitsa, pansi pa mapiko a akerubi.

8. Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pa malo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zace pamwamba pace.

9. Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa cakuno ca moneneramo, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo ziri komweko mpaka lero lino.

10. Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anacita cipangano ndi ana a Israyeli poturuka iwo m'Aigupto.

11. Ndipo ansembe anaturuka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;

2 Mbiri 5